Lachisanu, January 17
“Sipakufunika gulu lankhondo kapena mphamvu, koma mzimu wanga,” watero Yehova.—Zek. 4:6, 7.
Mu 522 B.C.E., adani a Ayuda anakwanitsa kuletsa ntchito yomanganso kachisi. Koma Zekariya anawatsimikizira kuti Yehova adzagwiritsa ntchito mzimu wake wamphamvu powathandiza kuti apitirizebe ntchito yawo ngakhale kuti panali mavuto. Mu 520 B.C.E., Mfumu Dariyo analamula kuti kachisiyo apitirize kumangidwa ndipo anapereka ndalama komanso anthu oti athandize pa ntchitoyo. (Ezara 6:1, 6-10) Yehova analonjeza anthu akewo kuti adzawathandiza ngati ataika ntchito yomanga kachisi pamalo oyamba. (Hag. 1:8, 13, 14; Zek. 1:3, 16) Atalimbikitsidwa ndi aneneriwo, Ayudawo anayambiranso kumanga kachisi mu 520 B.C.E. ndipo anamaliza pasanathe zaka 5. Popeza kuti Ayudawo ankaika zimene Mulungu ankafuna pamalo oyamba ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, iye anawathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi komanso kuwapatsa zimene ankafunikira. Zotsatira zake n’zakuti iwo anayamba kulambira Yehova mosangalala.—Ezara 6:14-16, 22. w23.11 15 ¶6-7
Loweruka, January 18
Tiziyenda moyenera potsatira chikhulupiriro chimene bambo wathu Abulahamu anali nacho.—Aroma 4:12.
Ngakhale kuti anthu ambiri anamvapo zokhudza Abulahamu, amadziwa zochepa zokhudza iye. Komabe inu mumadziwa zambiri zokhudza Abulahamu. Mwachitsanzo, mumadziwa kuti iye amatchedwa “bambo wa onse . . . amene ali ndi chikhulupiriro.” (Aroma 4:11) Ndiye mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi inenso ndingamakhulupirire kwambiri Yehova ngati mmene Abulahamu anachitira?’ Inde n’zotheka. Njira imodzi yomwe tingakhalire ndi chikhulupiriro ngati Abulahamu, ndi kuphunzira pa chitsanzo chake. Mulungu atamulamula, Abulahamu anasamukira kutali ndi dziko lakwawo, ankakhala m’matenti komanso anali wofunitsitsa kupereka mwana wake Isaki ngati nsembe. Zimene anachitazo zinasonyeza kuti iye ankakhulupirira kwambiri Yehova. Chikhulupiriro komanso ntchito zake zinachititsa kuti Yehova azisangalala naye komanso akhale mnzake. (Yak. 2:22, 23) Yehova amafuna kuti tonsefe, kuphatikizapo inuyo, tikhale naye pa ubwenzi. Choncho iye anauzira Paulo ndi Yakobo kuti alembe m’Baibulo chitsanzo cha Abulahamu. w23.12 2 ¶1-2
Lamlungu, January 19
Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule.—Yak. 1:19.
Alongo, muziphunzira kulankhula bwino ndi anthu. Akhristu amafunika kulankhula bwino ndi anthu. Pa nkhani imeneyi, Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anapereka malangizo amene ali mulemba lalero. Mukamamvetsera mosamala pamene ena akulankhula, mumasonyeza kuti mumaganizira anthu ena ndiponso kuwamvera chisoni. (1 Pet. 3:8) Ngati mukukayikira zoti mwamvetsa zimene munthu wina akunena kapena mmene akumvera mungachite bwino kumufunsa mafunso oyenera. Kenako muziganiza kaye musanalankhule. (Miy. 15:28) Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikufuna kulankhula ndi zoona komanso zolimbikitsa? Kodi zisonyeza ulemu komanso kukoma mtima? Muziphunzira kwa alongo olimba mwauzimu amene amalankhula bwino ndi anthu. (Miy. 31:26) Muziona mmene amalankhulira. Mukaphunzira kulankhula bwino ndi anthu, m’pamenenso muzigwirizana nawo kwambiri. w23.12 21 ¶12