DECEMBER 16-22
SALIMO 119:57-120
Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Zimene Tingachite Kuti Tizipirira Mavuto
(10 min.)
Tizipitiriza kuwerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu (Sl 119:61; w06 6/15 20 ¶2; w00 12/1 14 ¶3)
Tizilola kuti mavutowo atiyenge (Sl 119:71; w06 9/1 14 ¶4)
Tizidalira Yehova kuti atilimbikitse (Sl 119:76; w17.07 13 ¶3, 5)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova wandithandiza kupirira mavuto anga m’njira ziti?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Sl 119:96—Kodi n’kutheka kuti vesili limatanthauza chiyani? (w06 9/1 14 ¶5)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 119:57-80 (th phunziro 12)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Musonyezeni webusaiti yathu ya jw.org ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za webusaitiyi. (lmd phunziro 2 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni kuti adzamvetsere nkhani ya onse yotsatira. Gwiritsani ntchito vidiyo yamutu wakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (lmd phunziro 8 mfundo 3)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Chitsanzo. ijwbq 157—Mutu: Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zam’chilengedwe? (lmd phunziro 3 mfundo 3)
Nyimbo Na. 128
7. Yehova Amatithandiza Kupirira
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Kupirira kumatanthauza kusagonja tikakumana ndi mavuto. Kumaphatikizapo kukhalabe wolimba, kupitiriza kuona zinthu moyenera komanso kukhala ndi chiyembekezo kuti mayeserowo atha. Mkhristu akakhala wopirira, ‘sabwerera m’mbuyo’ kapena kufooka akakumana ndi mavuto. (Ahe 10:36-39) Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza kupirira mayesero.—Ahe 13:6.
Pa lemba lililonse mwa malemba omwe ali m’munsiwa, lembani mmene Yehova amatithandizira kupirira.
Onerani VIDIYO yakuti Muzipempherera Anthu Amene Akukumana ndi Mavuto. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
Kodi tingagwiritse ntchito bwanji jw.org kuti tidziwe zokhudza abale ndi alongo athu amene akukumana ndi mayesero?
Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti azipempherera ena, nanga ubwino wake ndi wotani?
Kodi kupempha Yehova kuti athandize Akhristu anzathu kupirira n’kofunika bwanji?
Kodi kupempherera ena kungatithandize bwanji kupirira mayesero amene tikukumana nawo?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 19 ¶14-20, bokosi patsamba 152