Masalimo
Pemphero la Davide.
17 Imvani dandaulo lolungama, inu Yehova. Mvetserani kulira kwanga kochonderera.+
Tcherani khutu ku pemphero langa limene likutuluka pamilomo yopanda chinyengo.+
3 Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+
Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+
Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+
4 Kunena za ntchito za anthu,
Ndakhala wosamala mwa kusunga mawu a pakamwa panu, kuti ndisatengere njira ya wachifwamba.+
6 Ine ndikuitana pa inu, chifukwa mudzandiyankha, inu Mulungu.+
Tcherani khutu kwa ine. Imvani mawu anga.+
7 Sonyezani kukoma mtima kosatha mwa kuchita zodabwitsa,+ inu Mpulumutsi wa anthu othawira kwa inu,
Amene akuthawa anthu ogalukira dzanja lanu lamanja.+
8 Ndisungeni monga mwana wa diso,+
Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu,+
9 Chifukwa cha anthu oipa amene akundipondereza.
Adani a moyo wanga atsala pang’ono kundipeza.+
10 Mitima yawo siimva chisoni,*+
Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.+
11 Tsopano adaniwo atizungulira, kulikonse kumene tingapite.+
Akutiyang’anitsitsa kuti atigwetse.+
12 Aliyense wa iwo akuoneka ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama.+
Akuonekanso ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama.
13 Nyamukani, inu Yehova, yang’anizanani naye maso ndi maso woipayo.+
M’gonjetseni. Pulumutsani moyo wanga kwa woipayo ndi lupanga lanu.+
14 Ndipulumutseni kwa anthu ndi dzanja lanu, inu Yehova,+
Ndipulumutseni kwa anthu a m’nthawi* ino,+ amene gawo lawo lili m’moyo uno.+
Anthu amene mimba zawo mwazidzaza ndi chuma chanu chobisika,+
Amene ali ndi ana aamuna ochuluka,+
Ndipo amakundikira ana awo chuma.+