Masalimo
33 Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova, inu nonse olungama.+
M’poyenera kuti owongoka mtima atamande Mulungu.+
3 Muimbireni nyimbo yatsopano.+
Muimbireni choimbira cha zingwe ndi mtima wonse ndi kufuula mosangalala.+
5 Iye amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.+
Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.+
6 Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+
Ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.+
7 Anasonkhanitsa madzi a m’nyanja ngati wachita kuwatchinga ndi khoma,+
Anaika madzi amphamvu m’nyumba zosungiramo zinthu.
8 Onse okhala padziko lapansi aope Yehova.+
Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.+
11 Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+
Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
12 Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+
Anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.+
16 Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+
Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+
17 Hatchi siingabweretse chipulumutso,+
Siingapulumutse munthu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+