Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.
87 Maziko a mzinda wa Mulungu ali m’mapiri opatulika.+
2 Yehova amakonda kwambiri zipata za Ziyoni+
Kusiyana ndi mahema onse a Yakobo.+
3 Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ [Seʹlah.]
4 Ine ndidzatchula Rahabi+ ndi Babulo+ monga ena mwa amene akundidziwa.
Ponena za Filisitiya,+ Turo ndi Kusi ine ndidzati:
“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+
5 Ponena za Ziyoni anthu adzati:
“Aliyense anabadwira mmenemo.”+
Ndipo Wam’mwambamwamba+ adzakhazikitsa mzinda umenewo.+
6 Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:+
“Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+ [Seʹlah.]
7 Kudzakhalanso oimba komanso ovina gule wovina mozungulira amene adzati:+
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”+