Levitiko
11 Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 2 “Uzani ana a Isiraeli kuti, ‘Zolengedwa zimene mungadye+ pa nyama zonse zimene zili padziko lapansi ndi izi: 3 Cholengedwa chilichonse pakati pa nyama, chimene chili ndi ziboda zogawanika zokhala ndi mpata pakati, chomwenso chimabzikula, n’chimene mungadye.+
4 “‘Koma pakati pa nyama zimene zimabzikula ndi zimene zili ndi ziboda zogawanika, izi zokha musadye: Ngamila, chifukwa imabzikula koma ziboda zake n’zosagawanika. Nyama imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu.+ 5 Ndiponso mbira,+ chifukwa imabzikula, koma ziboda zake n’zosagawanika. Ikhale yodetsedwa kwa inu. 6 Chimodzimodzinso kalulu,+ chifukwa amabzikula, koma ziboda zake n’zosagawanika. Akhale wodetsedwa kwa inu. 7 Komanso nkhumba,+ chifukwa ziboda zake n’zogawanika ndipo zili ndi mpata pakati, koma siibzikula. Ikhale yodetsedwa kwa inu. 8 Musadyeko nyama iliyonse ya zimenezi, ndipo nyamazi zikafa musamazikhudze.+ Zikhale zodetsedwa kwa inu.+
9 “‘Zimene mungadye pa zonse za m’madzi ndi izi: Chilichonse cha m’madzi+ chokhala ndi zipsepse ndi mamba,+ chopezeka m’nyanja ndi m’mitsinje mungadye. 10 Koma pa zamoyo za m’madzi zopezeka zambiri ndi pa zamoyo zina zonse za m’madzi, chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba, chopezeka m’nyanja ndi m’mitsinje, chikhale chonyansa kwa inu. 11 Zinthu zimenezi zikhale zonyansa kwa inu. Musamadye nyama yake iliyonse,+ ndipo zikafa zizikhalabe zonyansa kwa inu. 12 Chamoyo chilichonse cha m’madzi chimene chilibe zipsepse ndi mamba, chikhale chonyansa kwa inu.
13 “‘Pakati pa zolengedwa zouluka,+ izi zikhale zonyansa kwa inu. Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: Chiwombankhanga,+ nkhwazi ndi muimba wakuda. 14 Komanso mtundu uliwonse wa mphamba wofiira ndi mphamba wakuda,+ 15 ndi mtundu uliwonse wa khwangwala.+ 16 Musadyenso nthiwatiwa,+ kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi. 17 Ndiponso musadye nkhwezule, chiswankhono, mantchichi,+ 18 tsekwe, vuwo, muimba,+ 19 dokowe, sadzu, mleme+ ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 20 Tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, ta mapiko ndiponso ta miyendo inayi, tikhale tonyansa kwa inu.+
21 “‘Pa tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, ta mapiko ndiponso ta miyendo inayi, mungathe kudya tizilombo tokhalanso ndi miyendo italiitali yolumphira. Tokhati n’timene mungadye. 22 Tizilombo timene mungadyeto ndi iti: Mtundu uliwonse wa dzombe loyenda mitunda italiitali*+ ndi mitundu ina ya dzombe,+ mtundu uliwonse wa nkhululu, ndi mtundu uliwonse wa chiwala.+ 23 Koma tizilombo tina tonse timene timapezeka tambiri, ta mapiko ndiponso ta miyendo inayi, tikhale tonyansa+ kwa inu. 24 Tizilombo timeneti n’timene mungadzidetse nato. Aliyense wokhudza zolengedwa zimenezi zitafa azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 25 Ndipo aliyense wonyamula chilichonse mwa zolengedwa zimenezi chitafa, azichapa+ zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.
26 “‘Nyama iliyonse yokhala ndi chiboda chogawanika koma chosakhala ndi mpata pakati, imenenso siibzikula, ndi yodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza nyama yoteroyo azikhala wodetsedwa.+ 27 Pakati pa zamoyo zonse za miyendo inayi, chamoyo chilichonse chokhala ndi mapazi a zikhadabo n’chodetsedwa kwa inu. Aliyense wokhudza chamoyo chimenechi chitafa azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 28 Ndipo munthu wonyamula iliyonse ya nyama zimenezi itafa,+ azichapa zovala zake,+ ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Nyama zimenezi zikhale zodetsedwa kwa inu.
29 “‘Pa zamoyo zonse zokwawa padziko lapansi, zodetsedwa ndi izi:+ Mfuko, mbewa yoyenda modumpha+ ndi mtundu uliwonse wa buluzi. 30 Ndiponso nalimata, buluzi wamkulu, dududu, buluzi wa mumchenga ndi bilimankhwe. 31 Zamoyo zimenezi ndi zodetsedwa kwa inu pa zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri.+ Aliyense wokhudza zolengedwa zimenezi zitafa azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+
32 “‘Tsopano chamoyo chilichonse mwa zimenezi chikafa n’kugwera pa chinthu china chilichonse, chinthucho chizikhala chodetsedwa. Kaya ndi chiwiya chamtengo,+ chovala, chikopa,+ kapena chiguduli*+ chizikhala chodetsedwa. Chiwiya chilichonse chimene chimagwiritsidwa ntchito chiziikidwa m’madzi, koma chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo, kenako chizikhala choyera. 33 Chilichonse mwa zamoyo zimenezi chikagwera m’chiwiya chadothi,+ chilichonse chimene chili m’chiwiyacho chizikhala chodetsedwa, ndipo chiwiyacho muzichiphwanya.+ 34 Madzi a m’chiwiya chimenechi akagwera pachakudya chilichonse, chakudyacho chizikhala chodetsedwa. Ndipo chakumwa chilichonse chimene mungamwere m’chiwiya chilichonse, chikasakanikirana ndi madzi ochokera m’chiwiya chodetsedwa chija, chakumwacho chizikhala chodetsedwa. 35 Chilichonse mwa zamoyo zimenezi chikafa n’kugwera pachinthu chilichonse, chinthucho chizikhala chodetsedwa ndipo chiziphwanyidwa, kaya ndi uvuni kapena chokhazikapo mtsuko. Ziwiya zimenezi zadetsedwa ndipo zikhale zodetsedwa kwa inu. 36 Kasupe ndiponso dziwe ndi zokhazo zimene zizikhalabe zoyera, koma aliyense wokhudza cholengedwa chimene chafacho azikhala wodetsedwa. 37 Ndipo chilichonse mwa zolengedwa zimenezi chikafa n’kugwera pambewu iliyonse yoti mubzale, mbewuyo izikhalabe yoyera. 38 Koma mbewuyo ikathiridwa madzi ndipo chiwalo chilichonse cha nyama yakufayo n’kugwerapo, mbewuyo izikhala yodetsedwa kwa inu.
39 “‘Nyama iliyonse imene mwaloledwa kudya ikapezeka itafa, aliyense wokhudza nyama yakufayo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 40 Aliyense wakudya+ nyama yofa yokha azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Aliyense wonyamula nyama yakufayo azichapa zovala zake, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 41 Ndipo zamoyo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi zikhale zonyansa.+ Zimenezi musadye. 42 Pa zilombo zonse zimene zimapezeka zambiri padziko lapansi, musamadye chamoyo chilichonse chokwawa+ ndiponso chamoyo chilichonse cha miyendo inayi kapena cha miyendo yambiri, chifukwa zimenezi ndi zonyansa.+ 43 Musamadziipitse ndi zamoyo zilizonse zimene zimapezeka zambirizi ndipo musamadzidetse nazo ndi kukhala odetsedwa.+ 44 Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ Mudzipatule ndi kukhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+ Choncho musamadzidetse ndi chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi. 45 Ine ndine Yehova amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu.+ Muzikhala oyera,+ chifukwa ine ndine woyera.+
46 “‘Limeneli ndi lamulo lokhudza nyama, zolengedwa zouluka, zamoyo zonse za m’madzi+ ndi zamoyo zonse zapamtunda, 47 kuti muzisiyanitsa+ chodetsedwa ndi choyera komanso zamoyo zimene muyenera kudya ndi zimene simuyenera kudya.’”