2 Kenako Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda m’manja mwake.+ Anaperekanso kwa iye zina mwa ziwiya+ za m’nyumba ya Mulungu woona moti Nebukadinezara anazitengera kudziko la Sinara,+ kunyumba ya mulungu wake. Ziwiya zimenezi anakaziika m’nyumba ya mulungu wake yosungiramo chuma.+