Ekisodo 16:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndipo iye anawayankha kuti: “Ndi zimene Yehova wanena. Mawa tisunga sabata, sabata lopatulika la Yehova.+ Zimene mungaphike, phikani, ndipo zimene mungawiritse, wiritsani.+ Zotsala zonse muziike pambali ndi kuzisunga mpaka m’mawa.” Ekisodo 20:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo wokhala mumzinda wanu.+ Luka 23:56 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 56 Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira.+ Komabe pa tsiku la sabata+ anapuma malinga ndi chilamulo.
23 Ndipo iye anawayankha kuti: “Ndi zimene Yehova wanena. Mawa tisunga sabata, sabata lopatulika la Yehova.+ Zimene mungaphike, phikani, ndipo zimene mungawiritse, wiritsani.+ Zotsala zonse muziike pambali ndi kuzisunga mpaka m’mawa.”
10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo wokhala mumzinda wanu.+
56 Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira.+ Komabe pa tsiku la sabata+ anapuma malinga ndi chilamulo.