-
Levitiko 10:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara, kuti: “Musalekerere tsitsi lanu osalisamala,+ ndipo musang’ambe zovala zanu kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire khamu lonseli.+ Abale anu, nyumba yonse ya Isiraeli ndiwo alire chifukwa cha kuwononga ndi moto kumene Yehova wachita.
-
-
Numeri 8:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ndipo ndidzapereka Alevi kwa Aroni ndi ana ake monga operekedwa kuchokera mwa ana a Isiraeli.+ Aleviwo adzatumikira m’malo mwa ana a Isiraeli pachihema chokumanako,+ ndipo aziphimba machimo a ana a Isiraeli.+ Chifukwa cha utumiki wawowo, mliri sudzawagwera ana a Isiraeli pakuti sadzayandikira malo oyerawo.”
-