20 Mbadwa za Rubeni, mwana woyamba wa Isiraeli,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba malinga ndi mabanja awo, ndiponso potsata nyumba za makolo awo. Analemba amuna onse kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, aliyense woyenerera kupita kunkhondo.