11 Iye anayamba kulonjeza+ kuti: “Inu Yehova wa makamu, mukaona nsautso yanga, ine kapolo wanu wamkazi,+ ndi kundikumbukira,+ ndiponso ngati simudzaiwala kapolo wanu wamkazi ndi kum’patsa mwana wamwamuna, ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo lezala silidzadutsa m’mutu mwake.”+