-
2 Mafumu 17:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anapangana ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso+ zimene iye anali kuwachenjeza nazo. M’malomwake anayamba kutsatira mafano opanda pake+ ndipo iwowo nawonso anakhala opanda pake.+ Anatsatira mitundu imene inawazungulira, imene Yehova anawalamula kuti asamachite zofanana nayo.+
-
Yeremiya 32:35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Kuwonjezera apo anamangira Baala+ malo okwezeka m’chigwa cha mwana wa Hinomu.+ Anachita izi kuti azidutsitsa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto monga nsembe+ kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule zimenezi+ ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga kuchita chinthu chonyansa chimenechi,+ kuti Yuda achite tchimo.’+
-
-
-