16 “Mawa nthawi ngati ino ndikutumizira munthu kuchokera kudera la Benjamini,+ ndipo udzam’dzoze+ kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli. Iye adzapulumutsa anthu anga m’manja mwa Afilisiti,+ chifukwa ndaona kusautsika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”+