5 Kuwonjezera apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka.+ Anamanga nsanja+ pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina.+ Anakonzanso Chimulu cha Dothi+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zida+ zambiri ndi zishango.+