8 Inu mfumu dziwani kuti ife tinapita kuchigawo+ cha Yuda kunyumba ya Mulungu wamkulu.+ Kumeneko takapeza kuti nyumbayo akuimanga ndi miyala yochita kuigubuduzira pamalo ake ndiponso akuika matabwa m’makoma ake. Iwo akugwira ntchitoyo mwakhama ndipo ikupita patsogolo.