20Tsopano panali munthu wina wopanda pake+ dzina lake Sheba,+ mwana wamwamuna wa Bikiri, wafuko la Benjamini. Iye analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi kunena kuti: “Tilibe gawo mwa Davide, ndipo tilibe cholowa mwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu+ yake!”