Machitidwe 14:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzira+ ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’chikhulupiriro. Anali kuwauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”+ Aheberi 2:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ndiye chifukwa chake n’kofunika kuti tiganizire mozama, kuposa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva,+ kuti tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.+ Aheberi 12:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ndipo mwaiwaliratu langizo lokudandaulirani limene limakutchani ana,+ lakuti: “Mwana wanga, usapeputse chilango* cha Yehova, kapena kutaya mtima pamene iye akukudzudzula.+ Aheberi 12:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+
22 M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzira+ ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’chikhulupiriro. Anali kuwauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”+
2 Ndiye chifukwa chake n’kofunika kuti tiganizire mozama, kuposa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva,+ kuti tisatengeke pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro.+
5 Ndipo mwaiwaliratu langizo lokudandaulirani limene limakutchani ana,+ lakuti: “Mwana wanga, usapeputse chilango* cha Yehova, kapena kutaya mtima pamene iye akukudzudzula.+
11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+