24 “Koma amene akudzitamanda adzitamande pa chifukwa chakuti, amamvetsa bwino+ njira zanga ndipo amandidziwa, kuti ine ndine Yehova,+ amene ndimasonyeza kukoma mtima kosatha, ndimapereka ziweruzo ndi kuchita chilungamo padziko lapansi.+ Pakuti zinthu zimenezi zimandisangalatsa,”+ watero Yehova.