13 Taona! Yehova Mulungu wa makamu ndilo dzina+ la amene anapanga mapiri,+ analenga mphepo,+ amene amafotokozera munthu zimene akuganiza,+ amene amachititsa kuwala kwa m’bandakucha kukhala mdima+ ndiponso amene amaponda malo okwezeka a dziko lapansi.”+