Ekisodo 4:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?+ Hoseya 14:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Bwerera kwa Yehova ndi mawu osonyeza kulapa.+ Anthu nonsenu uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.+ Luka 21:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+ Aroma 10:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake+ kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera+ chikhulupiriro chake kuti apulumuke. Aheberi 13:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+
11 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndani, kapena ndani amapanga munthu wosalankhula, wogontha, woona kapena wakhungu? Kodi si ine, Yehova?+
2 Bwerera kwa Yehova ndi mawu osonyeza kulapa.+ Anthu nonsenu uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.+
15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+
10 Munthu amakhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake+ kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyera+ chikhulupiriro chake kuti apulumuke.
15 Kudzera mwa iye, tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu,+ yomwe ndi chipatso cha milomo yathu.+ Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.+