24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga ziunda zomenyerapo nkhondo+ kuti aulande,+ moti uperekedwa m’manja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu.+ Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri.+ Zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.+