3 Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindamo ndi kukhala pansi ku Chipata cha Pakati.+ Mayina a akalongawo anali Nerigali-sarezera, Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi, Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.