Oweruza 6:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Amidiyaniwo anayamba kusautsa Aisiraeli.+ Chifukwa cha kusautsidwa ndi Amidiyani kumeneku, ana a Isiraeli anadzikonzera malo apansi osungiramo zinthu m’mapiri. Anadzikonzeranso mapanga ndi malo ena ovuta kufikako kuti azithawirako.+ 1 Samueli 13:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndipo amuna a Isiraeli anaona kuti zinthu zawathina,+ chifukwa anthu onse anali atapanikizika. Anthuwo anapita kukabisala m’mapanga,+ m’maenje, kumatanthwe, m’zipinda za pansi ndi m’zitsime zopanda madzi.
2 Amidiyaniwo anayamba kusautsa Aisiraeli.+ Chifukwa cha kusautsidwa ndi Amidiyani kumeneku, ana a Isiraeli anadzikonzera malo apansi osungiramo zinthu m’mapiri. Anadzikonzeranso mapanga ndi malo ena ovuta kufikako kuti azithawirako.+
6 Ndipo amuna a Isiraeli anaona kuti zinthu zawathina,+ chifukwa anthu onse anali atapanikizika. Anthuwo anapita kukabisala m’mapanga,+ m’maenje, kumatanthwe, m’zipinda za pansi ndi m’zitsime zopanda madzi.