12 Inu Yehova, ndinu Mulungu wolungama.+ Ndikabweretsa dandaulo kwa inu, ndipo ndikalankhula za chiweruzo chanu, mumachita chilungamo. Koma n’chifukwa chiyani anthu oipa, zinthu zikuwayendera bwino?+ N’chifukwa chiyani onse ochita chinyengo amakhala opanda nkhawa iliyonse?