17 “‘Mwamuna akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake, n’kugona naye, chimenecho ndi chinthu chochititsa manyazi.+ Chotero onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo. Iye wavula mlongo wake ndipo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.