10 Iwo abwerera ku zolakwa zimene makolo awo+ anachita kalekale. Makolowo anakana kumvera mawu anga, m’malomwake anayamba kutsatira milungu ina kuti aitumikire.+ A m’nyumba ya Isiraeli ndi a m’nyumba ya Yuda aphwanya pangano langa limene ndinachita ndi makolo awo.+