Yesaya 32:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 kufikira mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+ ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso. Munda wa zipatsowo udzakhala ngati nkhalango yeniyeni.+ Yesaya 44:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pakuti ndidzapatsa madzi munthu waludzu,+ ndipo ndidzaika timitsinje tamadzi pamalo ouma.+ Ndidzatsanulira mzimu wanga pambewu yako+ ndi madalitso anga pa mbadwa zako. Ezekieli 39:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Sindidzawabisiranso nkhope yanga+ chifukwa panyumba ya Isiraeli, ndidzatsanulirapo mzimu wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” Machitidwe 2:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 ‘“Ndipo m’masiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga+ pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+
15 kufikira mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+ ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso. Munda wa zipatsowo udzakhala ngati nkhalango yeniyeni.+
3 Pakuti ndidzapatsa madzi munthu waludzu,+ ndipo ndidzaika timitsinje tamadzi pamalo ouma.+ Ndidzatsanulira mzimu wanga pambewu yako+ ndi madalitso anga pa mbadwa zako.
29 Sindidzawabisiranso nkhope yanga+ chifukwa panyumba ya Isiraeli, ndidzatsanulirapo mzimu wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
17 ‘“Ndipo m’masiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzatsanulira mbali ya mzimu wanga+ pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. Anyamata anu adzaona masomphenya, ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+