13 Komabe, tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale okondedwa ndi Yehova. Tiyenera kutero chifukwa Mulungu anakusankhani+ kuchokera pachiyambi kuti mudzapulumuke mwa kukuyeretsani+ ndi mzimu,+ ndiponso mwa chikhulupiriro chanu m’choonadi.+