18 Cholinga cha pangano limeneli n’chakuti, pakati panu pasapezeke mwamuna, mkazi, banja kapena fuko limene mtima wake ukupatuka kusiyana ndi Yehova Mulungu wathu, ndi kupita kukatumikira milungu ya mitundu inayo,+ kuti pakati panu pasapezeke muzu wotulutsa chomera chakupha ndi chitsamba chowawa.+