-
Genesis 40:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Tsiku lachitatulo linali tsiku lokumbukira kubadwa+ kwa Farao. Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa mʼndende* mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika mkate, nʼkuwaimiritsa pamaso pa antchito ake onse. 21 Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera zakumwa uja, moti anapitiriza ntchito yake yoperekera zakumwa kwa Farao.
-