-
Genesis 41:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndiyeno ndinalotanso maloto ena. Ndinalota ngala 7 za tirigu, zokhwima ndi zooneka bwino, zikutuluka paphesi limodzi.+ 23 Pambuyo pake ndinaonanso ngala zina 7 zikutuluka ndipo zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa. 24 Ndiyeno ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zooneka bwinozo. Ndinafotokozera malotowa ansembe amatsenga,+ koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kumasulira.”+
-