Genesis 1:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Komanso, Mulungu anawadalitsa nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi+ ndipo muziliyangʼanira.+ Muyangʼanirenso+ nsomba zamʼnyanja ndi zamoyo zouluka mumlengalenga, komanso chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi.” Genesis 10:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Mabanja a ana a Nowa ndi amenewa malinga ndi mibadwo yawo komanso mitundu yawo. Kuchokera mwa anthu amenewa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa Chigumula.+
28 Komanso, Mulungu anawadalitsa nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi+ ndipo muziliyangʼanira.+ Muyangʼanirenso+ nsomba zamʼnyanja ndi zamoyo zouluka mumlengalenga, komanso chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi.”
32 Mabanja a ana a Nowa ndi amenewa malinga ndi mibadwo yawo komanso mitundu yawo. Kuchokera mwa anthu amenewa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa Chigumula.+