12 Mulungu anawonjezera kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndikuchita ndi inu komanso ndi chamoyo chilichonse chimene muli nacho, mpaka mibadwo yonse ya mʼtsogolo. 13 Ndaika utawaleza wanga mumtambo, ndipo ukhala chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi dziko lapansi.