42 Rabeka atauzidwa zimene mwana wake wamkulu Esau ananena, nthawi yomweyo anaitanitsa mwana wake wamngʼono Yakobo nʼkumuuza kuti: “Mʼbale wako Esau akufuna akuphe pobwezera zimene unamuchitira. 43 Choncho uchite zimene ndikuuze mwana wanga. Nyamuka, thawira kwa mchimwene wanga Labani, ku Harana.+