-
Ekisodo 28:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Zovala zoti apange ndi izi: chovala pachifuwa,+ efodi,+ malaya akunja odula manja,+ mkanjo wamandalasi, nduwira+ ndi lamba wapamimba.+ Aroni mʼbale wako ndi ana ake awapangire zovala zopatulikazi, kuti atumikire monga ansembe anga. 5 Anthu alusowo agwiritse ntchito golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.
-