-
Ekisodo 4:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Zitatero, Yehova anakwiyira kwambiri Mose ndipo anati: “Kodi si paja Aroni+ Mlevi uja ndi mʼbale wako? Ndikudziwa kuti amalankhula bwino kwambiri. Ndiponso, iye ali mʼnjira kudzakuchingamira. Akakuona, adzakondwera kwambiri mumtima mwake.+ 15 Choncho ukalankhule naye ndi kumuuza zoti akanene.+ Ineyo ndidzakhala ndi iwe pamodzi ndi iye mukamakalankhula+ ndipo ndidzakuuzani zochita. 16 Iyeyo ndi amene azikalankhula kwa anthu mʼmalo mwa iwe. Choncho adzakhala wokulankhulira, ndipo iwe udzakhala ngati Mulungu kwa iye.+
-