-
Machitidwe 7:30-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Patapita zaka 40, mngelo anaonekera kwa iye mʼchipululu paphiri la Sinai, pachitsamba chaminga chimene chinkayaka moto.+ 31 Mose ataona zimenezi, anadabwa kwambiri. Koma pamene ankayandikira kuti aonetsetse, anamva mawu a Yehova* akuti, 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo.’+ Mose anayamba kunjenjemera ndipo sanafunenso kupita pafupi ndi chitsambacho kuti akaonetsetse. 33 Yehova* anamuuza kuti, ‘Vula nsapato zako, chifukwa malo waimawo ndi malo oyera. 34 Ine ndaona kuti anthu anga omwe ali ku Iguputo akuzunzidwa kwambiri. Ndamva kubuula kwawo+ ndipo ndabwera kudzawapulumutsa. Ndiye ndikufuna ndikutume ku Iguputo.’
-