29 Ndiyeno Mose anauza Hobabu mwana wa mpongozi wake Reueli+ wa ku Midiyani, kuti: “Tikusamukira kumalo amene Yehova anati, ‘Ndidzawapereka kwa inu.’+ Tiyeni tipite limodzi,+ ndipo tidzakuchitirani zabwino, chifukwa Yehova analonjeza Aisiraeli zinthu zabwino.”+