-
Levitiko 24:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti akubweretsere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 3 Aroni azikhazika nyale kunja kwa katani ya Malo Oyera Koposa mʼchihema chokumanako. Nyalezo ziziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka mʼmawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse.
-