-
Ekisodo 31:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Muzisunga Sabata chifukwa ndi lopatulika kwa inu.+ Aliyense wosatsatira lamulo lokhudza sabata ayenera kuphedwa ndithu. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsikuli ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 15 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa.
-