-
Levitiko 6:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ngati wachimwa ndipo wapalamula mlandu, azibweza zinthu zimene anabazo, kapena zinthu zimene analanda mwachinyengo, kapena chimene anamʼsungitsa, kapena chinthu chotayika chimene anatola, 5 kapena chilichonse chimene analumbira monama. Azibweza chinthucho+ nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo ake 5. Azibweza zimenezi kwa mwiniwake pa tsiku limene wapezeka kuti ndi wolakwa.
-
-
Numeri 5:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi wachita machimo alionse amene anthu amachita, nʼkuchita zinthu mosakhulupirika pamaso pa Yehova, munthu ameneyo wapalamula mlandu.+ 7 Munthuyo aziulula+ tchimo limene wachita. Azipereka malipiro onse a mlandu wake, komanso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a malipirowo.+ Azipereka malipirowo kwa munthu amene wamulakwira.
-