-
Deuteronomo 14:12-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Koma mbalame izi ndi zimene simuyenera kudya: chiwombankhanga, nkhwazi, muimba wakuda,+ 13 mphamba wofiira, mphamba wakuda ndi mtundu uliwonse wa kamtema. 14 Simuyeneranso kudya mtundu uliwonse wa khwangwala, 15 nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi, 16 nkhwezule, mantchichi, tsekwe, 17 vuwo, muimba, chiswankhono, 18 dokowe, sadzu, mleme ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 19 Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri nʼtodetsedwanso kwa inu. Timeneti simuyenera kudya.
-