-
Levitiko 7:1-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 “‘Lamulo la nsembe yakupalamula+ ndi ili: Nsembeyi ndi yopatulika koposa. 2 Nyama ya nsembe yakupalamula aziiphera pamalo amene amaphera nyama ya nsembe yopsereza, ndipo magazi ake+ aziwazidwa mbali zonse za guwa lansembe.+ 3 Azipereka mafuta ake onse,+ kuphatikizapo mchira wamafuta, mafuta okuta matumbo, 4 impso ziwiri zimene zili pafupi ndi chiuno komanso mafuta okuta impsozo. Azichotsanso mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+
-