-
Levitiko 15:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ ndipo azibwera nazo pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako, nʼkuzipereka kwa wansembe. 15 Ndiyeno wansembe azipereka nsembe mbalamezo, imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza. Wansembe azimuphimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha nthenda yake yakukhayo.
-