-
Numeri 15:22-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Koma mukalakwitsa zinthu nʼkulephera kusunga malamulo onsewa amene Yehova walankhula kudzera mwa Mose, 23 zonse zimene Yehova wakulamulani kudzera mwa Mose, kuchokera pa tsiku limene Yehova analamula mpaka mʼtsogolo mʼmibadwo yanu yonse, 24 ngati mwalakwitsa mosazindikira, ndipo gulu lonselo silinadziwe, gulu lonselo lizikapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzikapereka nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ Muzikaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale nsembe yamachimo.+
-