-
Deuteronomo 11:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno mukadzamvera mokhulupirika malamulo anga amene ndikukupatsani lero, komanso kukonda Yehova Mulungu wanu nʼkumamutumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 14 ndidzakupatsaninso mvula pa nthawi yake mʼdziko lanu, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ndipo mudzakolola mbewu zanu nʼkukhala ndi vinyo watsopano komanso mafuta.+ 15 Ndidzameretsa msipu mʼdziko lanu kuti ziweto zanu zidye, ndipo inu mudzadya nʼkukhuta.+
-