Deuteronomo 28:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Yehova adzakutsegulirani kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatseni mvula pa nyengo yake+ mʼdziko lanu ndi kudalitsa chilichonse chimene mukuchita. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inuyo simudzafunika kukongola kanthu kwa iwo.+ Yesaya 30:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munadzala munthaka,+ ndipo chakudya chochokera munthakayo chidzakhala chochuluka komanso chopatsa thanzi.*+ Pa tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+ Ezekieli 34:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Nkhosazo komanso malo ozungulira phiri langa adzalandira madalitso+ ndipo ndidzachititsa kuti mvula igwe pa nthawi yake. Madalitso adzagwa ambiri ngati mvula.+ Yoweli 2:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Inu ana aamuna a Ziyoni sangalalani chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera,Ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi,Mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+
12 Yehova adzakutsegulirani kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatseni mvula pa nyengo yake+ mʼdziko lanu ndi kudalitsa chilichonse chimene mukuchita. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inuyo simudzafunika kukongola kanthu kwa iwo.+
23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munadzala munthaka,+ ndipo chakudya chochokera munthakayo chidzakhala chochuluka komanso chopatsa thanzi.*+ Pa tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+
26 Nkhosazo komanso malo ozungulira phiri langa adzalandira madalitso+ ndipo ndidzachititsa kuti mvula igwe pa nthawi yake. Madalitso adzagwa ambiri ngati mvula.+
23 Inu ana aamuna a Ziyoni sangalalani chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera,Ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi,Mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+