-
Deuteronomo 1:34-38Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Nthawi yonseyi Yehova ankamva zimene munkanena ndipo anakwiya kwambiri, moti analumbira kuti,+ 35 ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mʼbadwo woipa uwu amene adzaone dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+ 36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune. Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzapereka dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+ 37 (Ngakhale inenso Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu, ndipo anati, “Iwenso sukalowa mʼdziko limeneli.+ 38 Yoswa mwana wa Nuni, amene akukutumikira+ ndi amene akalowe mʼdzikomo.+ Umulimbitse,*+ chifukwa ndi amene adzatsogolere Aisiraeli pokatenga dzikolo kukhala lawo.”)
-