-
Ekisodo 37:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe. Mulitali mwake linali masentimita 45, mulifupi mwake masentimita 45. Mbali zake zonse 4 zinali zofanana, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 90. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.*+ 26 Analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo.
-