-
Genesis 48:17-19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse. Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu nʼkuliika pamutu pa Manase. 18 Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba+ ndi uyu. Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19 Koma bambo akewo anapitiriza kukana nʼkunena kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu. Koma mngʼono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri nʼkupanga mitundu ya anthu.”+
-